Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Numeri 9:20 - Buku Lopatulika Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa Kachisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo. |
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa chihema amakhala m'chigono.
Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.
Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo.
Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.