Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 5:29 - Buku Lopatulika

Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Limeneli ndilo lamulo la za nsanje, pamene mkazi azembera mwamuna wake, nadziipitsa, ngakhale kuti ali m'manja mwa mwamuna wakeyo,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“ ‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake,

Onani mutuwo



Numeri 5:29
12 Mawu Ofanana  

Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Ichi ndi chilamulo cha nyama, ndi cha mbalame, ndi cha zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi cha zamoyo zonse zakukwawa pansi;


Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.


Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi:


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,


pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.


Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukire kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.


Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.


kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.