Numeri 5:15 - Buku Lopatulika15 pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 mwamunayo abwere ndi mkazi wakeyo kwa wansembe. Ndipo aperekere nsembe ya ufa wabarele wokwanira kilogaramu limodzi. Asathirepo mafuta kapena lubani pa nsembeyo, poti ndi chopereka cha chakudya choperekera nsanje, nsembe yotsutsa munthu, yoperekedwa kuti tchimo lakelo lizidziŵika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’ ” Onani mutuwo |