Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukire kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Tsono amlumbiritse mkaziyo kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sadagone nawe, ndipo ngati sudachite kanthu kokuipitsa pamene unali m'manja mwa mwamuna wako, madzi oŵaŵa ali apaŵa usatenge nawo matemberero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:19
5 Mawu Ofanana  

Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,


Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.


Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa