Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Mkaziyo amuimike pamaso pa Chauta ndi kummasula tsitsi, ndipo aike m'manja mwake nsembe yaufa yachikumbutso, chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Wansembeyo atenge madzi oŵaŵa m'manja mwake, madzi odzetsa matemberero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:18
18 Mawu Ofanana  

Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse.


ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Ndipo azing'amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m'mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!


pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.


natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi mu chihema, wansembeyo nalithire m'madzimo.


Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukire kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.


ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.


Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.


Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.


kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa