Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.
Numeri 4:30 - Buku Lopatulika Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, aliyense amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano. |
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.
Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.
Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake;
Ichi ndi cha Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako;
Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.