Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.
Numeri 32:9 - Buku Lopatulika Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo atapita ku chigwa cha Esikolo, nakaona dzikolo, adatayitsa mtima Aisraele, pakuŵauza kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa. |
Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.