Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 13:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ndipo adafika ku chigwa cha Esikolo, nathyolako nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa, ndipo aŵiri mwa iwowo adainyamula mopika. Adatengakonso makangaza ndi nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 13:23
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Malowa anawatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsangolo ana a Israele analichekako.


Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.


dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi;


Ndipo pambuyo pake kunali kuti anakonda mkazi m'chigwa cha Soreki, dzina lake ndiye Delila.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa