Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.
Numeri 32:16 - Buku Lopatulika Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu mizinda; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono iwo adasendera kwa Mose namuuza kuti, “Poyamba mutilole kuti timange kuno makola a nkhosa zathu, ndi mizinda yoti ana athu azikhalamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu. |
Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.
Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m'chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.
koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.
Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m'mizinda yanu imene ndinakupatsani;
Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; ndipo anadza ndi mafumu a anthu, anachita chilungamo cha Yehova, ndi maweruzo ake ndi Israele.