Numeri 32:13 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adaŵayendetsa m'chipululu muja zaka makumi anai, mpaka udatha mbadwo wonse umene udachimwira Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha. |
Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.
Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.
Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.
Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;