Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 107:4 - Buku Lopatulika

4 Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu; osapeza mzinda wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu; osapeza mudzi wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ena adasokera m'chipululu, osapeza njira yopita ku mzinda woti akakhalemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu, osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 107:4
11 Mawu Ofanana  

Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.


Atsanulira chimpepulo pa akulu, nawasokeretsa m'chipululu mopanda njira.


Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.


Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.


Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'chipululu.


Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.


Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso.


amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;


(amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.


Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa