Numeri 32:12 - Buku Lopatulika koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaone dzikolo, kupatula Kalebe yekha mwana wa Yefune, Mkenizi uja, ndi Yoswa mwana wa Nuni, chifukwa iwoŵa ndiwo adatsata Chauta kwathunthu.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ |
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.
simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.
Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.