Numeri 3:19 - Buku Lopatulika Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amuramu ndi Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amuramu ndi Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Kohati potsata mabanja ao ndi aŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. |
A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamiti-Ezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahaziyoti;
Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yowele mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; ndi a Ageresoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;
Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu.
Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;
Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.