Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.
Numeri 26:51 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chiŵerengero chonse cha Aisraele chinali 601,730. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. |
Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.
Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.
inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.
Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.