Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.
Numeri 26:12 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana aamuna a Simeoni potsata mabanja ao ana aamuna a Simeoni anali aŵa: Nemuwele anali kholo la banja la Anemuele. Yamini anali kholo la banja la Ayamini. Yakini anali kholo la banja la Ayakini. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini; |
Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.
Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi.
Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.
Ndi ana aamuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amenewo ndiwo mabanja a Simeoni.
A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;