Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:22 - Buku Lopatulika

22 A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mwa zidzukulu za Simeoni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:22
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.


Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.


Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.


Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:


owerengedwa ao a fuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.


owerengedwa ao a fuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.


Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa