Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.
Numeri 25:2 - Buku Lopatulika popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akaziwo ankaitana amuna ku nsembe za milungu yao, ndipo amunawo ankadya nawo, ndi kumapembedza milungu yaoyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo. |
Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.
Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.
Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.
Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.
Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera, nimwa vinyo wa nsembe yao yothira? Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.
Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsere mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,
Mukalakwira chipangano cha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.
osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.