Numeri 24:24 - Buku Lopatulika Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zombo zidzabwera kuchokera ku Kitimu, zidzaononga Asuri ndi Eberi. Kitimu nayenso adzaonongeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu; kupondereza Asuri ndi Eberi, koma iwonso adzawonongeka.” |
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.
Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo.
Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.
Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki.
Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika.
Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza.
Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, ndipo zinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.
Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.
Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
Tandionetsani Ine rupiya latheka. Chithunzithunzi ndi cholemba chake ncha yani? Anati iwo, Cha Kaisara.
Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.