Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:48 - Buku Lopatulika

48 Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Tikamlekerera chomwechi, anthu onse adzamkhulupirira, ndipo Aroma adzabwera nkudzatiwonongera malo athu oyeraŵa ndiponso mtundu wathuwu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:48
19 Mawu Ofanana  

Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.


Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo aliyense amene mukampeze, itanani kuukwatiku.


Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.


Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.


Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa