Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.
Numeri 21:23 - Buku Lopatulika Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Sihoni sadalole kuti Aisraele adutse dziko lake. Adasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi, napita kukamenyana nkhondo ndi Aisraele kuchipululu, ndipo adafika ku Yahazi, namenyana ndi Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli. |
Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.
Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.
Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.
Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira.
tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;
Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele.