Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 20:20 - Buku Lopatulika

Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Edomu adaŵayankha kuti, “Simudutsa ai.” Pamenepo Edomu adatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu kukalimbana ndi Aisraele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Edomu anayankhanso kuti, “Musadutse.” Kenaka Edomu anatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu komanso lamphamvu.

Onani mutuwo



Numeri 20:20
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.


Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;


Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.


Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira.


pamenepo Israele anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati padziko lanu; koma mfumu ya Edomu siinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Mowabu; nayenso osalola; ndipo Israele anakhala mu Kadesi.


Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele.