Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Motero Esau adadana naye Yakobe chifukwa choti m'malo modalitsa iyeyo, bambo wake adadalitsa Yakobe. Ndipo adati, “Nthaŵi yakuti ndilire maliro a bambo wanga ili pafupi, pamenepo ndidzamupha Yakobeyu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:41
34 Mawu Ofanana  

Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.


Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.


Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.


Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.


Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.


Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.


Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.


Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.


Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.


Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m'galeta, namuika m'galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.


Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.


Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga; polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wake.


Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta, kulanda mzinda wolimba nkosavuta; makangano akunga mipiringidzo ya linga.


zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.


Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.


Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;


Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa