Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali.
Numeri 2:29 - Buku Lopatulika Ndi fuko la Nafutali: ndi kalonga wa ana a Nafutali ndiye Ahira mwana wa Enani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi fuko la Nafutali: ndi kalonga wa ana a Nafutali ndiye Ahira mwana wa Enani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pabwere fuko la Nafutali, limene mtsogoleri wake ndi Ahira mwana wa Enani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani. |
Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ichi ndi chopereka cha Ahira mwana wa Enani.