Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
Numeri 19:6 - Buku Lopatulika Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yaikazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yamsoti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wansembe atenge mtengo wa mkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kamlangali, ndipo zonsezo aziponye m'moto m'mene ng'ombe ija ikunyekamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. |
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.
pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;
Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;
natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pamadzi oyenda;