Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 14:4 - Buku Lopatulika

4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 wansembe alamule anthu kuti wodwala amene akuti ayeretsedweyo, amtengere mbalame zamoyo ziŵiri zimene Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali ndi kanthambi ka hisope.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 14:4
11 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.


Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.


Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.


ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pamadzi oyenda;


natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pamadzi oyenda;


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.


Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yaikazi.


Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa