Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Numeri 19:20 - Buku Lopatulika Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Koma munthu woipitsidwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo achotsedwe pakati pa msonkhano, pakuti waipitsa malo opatulika a Chauta. Ameneyo ndi woipitsidwa chifukwa sadamuwaze madzi oyeretsera aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. |
Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.
Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa chihema changa ali pakati pao.
Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.
Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.
Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.