Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.
Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova?
Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.
Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.
Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako aamuna.