Numeri 18:9 - Buku Lopatulika9 Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako aamuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako amuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. Onani mutuwo |
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.