Numeri 18:11 - Buku Lopatulika11 Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Zinanso zanu ndi izi: zopereka zao zamphatso, ndi zopereka zoweyula za Aisraele. Zimenezi ndazipereka kwa iwe, kwa ana ako aamuna, ndi kwa ana ako aakazi amene ali ndi iwe, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Munthu aliyense amene ali wosaipitsidwa angathe kudyako. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako. Onani mutuwo |