Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 6:18 - Buku Lopatulika

18 Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ana onse aamuna a Aroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, monga kudalembedwa kuti zidzatero nthaŵi zonse pa mibadwo yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 6:18
19 Mawu Ofanana  

Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.


akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.


Naike dzanja lake pamutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.


Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,


Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.


Muzizidya izi monga zopatulika kwambiri; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.


Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?


popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa