Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Numeri 15:34 - Buku Lopatulika Ndipo anayamba wamsunga, popeza sichinanenedwe choyenera kumchitira iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anathanga wamsunga, popeza sichinanenedwa choyenera kumchitira iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adamponya m'ndende chifukwa choti sankadziŵa bwino zoti amchite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. |
Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;
Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.