Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 18:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Yetero mpongozi wake wa Mose ataona zonse zimene Moseyo ankachita, adafunsa kuti, “Kodi zonse zimene mukuchitira anthuzi nzotani? Chifukwa chiyani mukukhala nokha pano, pamene anthu akubwerabe kwa inu kuyambira m'maŵa mpaka usiku?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:14
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima panjira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumzinda uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele.


Ndipo kunatero kuti m'mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo.


Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;


Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.


Ndipo anayamba wamsunga, popeza sichinanenedwe choyenera kumchitira iye.


Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa