Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
Numeri 15:27 - Buku Lopatulika Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yamsoti ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ngati munthu mmodzi alakwa mosadziŵa, apereke mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. |
Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;