Numeri 15:22 - Buku Lopatulika Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Koma mwina mutha kulakwa mosadziŵa, osasunga malamulo onse amene Chauta adauza Mose, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, |
Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;
Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;
Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.
ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova analamula, ndi kunkabe m'mibadwo yanu;
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.