Kudzatero ndi ng'ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.
Numeri 15:10 - Buku Lopatulika Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pachopereka cha chakumwa mupereke vinyo wokwanira malita aŵiri, kuti ikhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. |
Kudzatero ndi ng'ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.
ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.
abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini.
ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.
Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.