Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 15:9 - Buku Lopatulika

9 abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 muperekere kumodzi ndi ng'ombeyo chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta okwanira malita aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:9
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m'maso mwake; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.


kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.


Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.


Ndi pazikondwerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.


Momwemo apereke mwanawankhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.


ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.


ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.


Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.


Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika;


Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.


Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;


ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;


Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.


pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.


Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa