Numeri 15:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. Onani mutuwoBuku Lopatulika9 abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 muperekere kumodzi ndi ng'ombeyo chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta okwanira malita aŵiri. Onani mutuwo |
Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika.