Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 15:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pachopereka cha chakumwa mupereke vinyo wokwanira malita aŵiri, kuti ikhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.’

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:10
5 Mawu Ofanana  

Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere.


Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”


pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri.


ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.


Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa