Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 15:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:5
18 Mawu Ofanana  

Ndiponso zidachuluka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iliyonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka.


m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka paguwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.


Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.


ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.


Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.


Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.


Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.


Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;


akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova;


Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


Kudzatero ndi ng'ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.


Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini.


Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.


Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.


Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;


Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.


Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa