Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 15:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:5
18 Mawu Ofanana  

Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza. Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso.


Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.


Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.


Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa.


Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire! Mfumu indilowetse mʼchipinda chake. Ife timasangalala ndi kukondwera nawe, tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo. Amachita bwinotu potamanda iwe!


“ ‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema.


Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka.


“ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, choperekacho chikhale nkhosa yayimuna kapena yayikazi yopanda chilema.


Ngati apereka nsembe ya mwana wankhosa, abwere naye pamaso pa Yehova.


Taonani chikoka ndi kukongola kwawo! Tirigu adzasangalatsa anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere.


“Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka,


Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka.


Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova.


Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse.


Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga.


Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa