Numeri 13:32 - Buku Lopatulika
Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu.
Onani mutuwo
Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu.
Onani mutuwo
Choncho adasimbira Aisraelewo zoipa za dzikolo zimene adakaziwona, adati, “Dziko limene tidakalizondalo ndi dziko limene limaononga anthu ake. Ndipo anthu onse amene tidaŵaona kumeneko ngaataliatali.
Onani mutuwo
Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali.
Onani mutuwo