Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 12:16 - Buku Lopatulika

Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake anthu aja adanyamuka ku Hazeroti nakamanga mahema ao ku chipululu cha Parani.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pambuyo pake anthu ananyamuka ku Heziroti ndi kukamanga mʼchipululu cha Parani.

Onani mutuwo



Numeri 12:16
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.


Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.


Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.


Kuchokera ku Kibroti-Hatava anthuwo anayenda kunka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti.


Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.


Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.


Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga mu Ritima.


Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.