Numeri 11:8 - Buku Lopatulika Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ankapita kukatola manayo, namapera pa mphero kapena kusinja mu mtondo, ndipo ankaphika, namapangira makeke. Kukoma kwake kunali ngati makeke ophika ndi mafuta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi. |
Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.
Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya.