Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 25:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Tsiku lina Yakobe adaphika nyemba zofiira, Esau nkubwera kuchokera kuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:29
10 Mawu Ofanana  

ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.


Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.


Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.


Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m'funga mwake, nadza, nazichekerachekera m'nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe.


Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasowa.


Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.


Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.


Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa