Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 6:31 - Buku Lopatulika

31 Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Makolo athu ankadya mana m'chipululu muja, monga Malembo akunenera kuti, ‘Ankaŵapatsa chakudya chochokera Kumwamba kuti adye.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:31
14 Mawu Ofanana  

ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.


Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamane mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.


Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.


Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.


Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.


Makolo anu adadya m'chipululu, ndipo adamwalira.


Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.


nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;


Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.


Koma m'mawa mwake mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa