Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 11:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthu ankapita kukatola manayo, namapera pa mphero kapena kusinja mu mtondo, ndipo ankaphika, namapangira makeke. Kukoma kwake kunali ngati makeke ophika ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:8
9 Mawu Ofanana  

Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala.


Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ”


Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi.


Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma.


Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo.


Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”


Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa