Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziocha, ochani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:23
16 Mawu Ofanana  

Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;


ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;


Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.


Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.


Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.


musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;


Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.


Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola.


Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.


Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.


Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa