Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
Numeri 10:14 - Buku Lopatulika Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Otsata mbendera ya zithando za fuko la Yuda ndiwo adayamba kunyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Nasoni mwana wa Aminadabu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu. |
Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;
Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda: