Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.
Numeri 1:47 - Buku Lopatulika Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alevi okha sadaŵaŵerengere kumodzi ndi enawo, potsata banja la makolo ao, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena. |
Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.
Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse mu Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.
Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.
Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.