Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 1:36 - Buku Lopatulika

A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mwa zidzukulu za Benjamini adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

Onani mutuwo



Numeri 1:36
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.


Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.


Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.


ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;


owerengedwa ao a fuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.


owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.


Mwa fuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'mizinda tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala mu Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.